Amema alimi kuyamba kugwiritsira ntchito layimu
Pamene alimi ambiri akudandaula ndi kukwera mtengo wa fetereza mdziko muno, mkulu wa kampani yopanga layimu m’boma la Balaka ya Balaka Limeworks Supply Company (BLISCOL) walimbikitsa alimi kuti nthawi yakwana yoti aganizire zoyamba kugwiritsa ntchito layimu pa ulimi wawo.
A Abdul Pillane afotoza kuti anthu ambiri mdziko muno samadziwa ntchito zina za layimu kupatula kugwiritsidwa ntchito yopentera nyumba ndi zinthu zina.
“Ambiri samadziwa kuti layimu amatha kugwiritsidwa ntchito ngati mchere wowonjezera chonde mu nthaka. Kumbali ya ife, tili ndi layimu wa mitundu iwiri ya zaulimi yomwe pa chingerezi timayitchula kuti Calcium ndi Dolomite. Dolomite ndi layimu amene amatha kuwonjezera chonde mu nthaka pomwe Calcium ndiamene amathandizira kukhazikitsa bata mbali ya michere yopezeka mu nthaka kuti mbewu zikule bwino,” anatero a Pillane.
Pamenepa iwo anapempha boma makamaka alangizi a zaulimi kuti ayambe kumapereka upangiri kwa alimiwa kuti ayambe kumagwiritsa ntchito layimu ndicholinga choti adzitha kukolola zochuluka.
Mwachitsanzo a Pillane anati alangiziwa atha kumawunikira alimiwa zakufunikira komayezetsa dothi la mu nthaka mwawo kuti adziwe za kuchuluka kapena mtundu wa layimu amene akuyenera kugwiritsa ntchito.